Home / Languages / Chichewa / Sunnah of Musaafahah – Chichewa

Sunnah of Musaafahah – Chichewa

Asilamu awiri atakumana. Patatha miyedzi iwiri kapena itatu mu lock down. Zoona zake ndi chisangalaro komanso chikodwelero ndiye nkhani ndiyakuti kugwirana manja wina ndi mnzake monga mmene machitidwe amtumiki wathu ( Sallalahu alayhi wa sallam) sunnah. Monga omutsatira masahaba Radhiyallahu anhum amkachitira. Nthawi iti! Nthawi pamene, Munthu wina ndi mnzake msilamu akamagwirana manja. Mulungu Allah Ta’ala amawasangalalira, komanso kuwakhululukira awo. Zomwe zimapangitsa matchimo awo kugwa kapena kupululuka ngati masamba amapangira kuchokera mmitengo.

Iyi ndi Nthawi yomwe imaonetsa anthu okhulupilira Eni Eni. Sangaitaye kapena kuiononkha sunnah ya mtumiki okondedwa Sallalahualayhiwasallam ayigwira moyilemekedzeka.
Palibe chomwe chingamuletse kuitsatira njira ya mtumiki (sunnah) Sallalahualayhiwasallam

Kupatura anthu osaganidza komanso othaika amene angaitaye njira ya mtumiki sallalahu Alayhi wasallam ogwirana manja.

Sizingakhale kapena sizingatheke kukhara Munthu omukonda mtumiki Muhammad sallalahu Alayhi wasallam akuwasathira zochita anthu osakhulupilira akunja Kwa chisilamu.

عَنْ أَبِي هُرَيْرَةَ قَالَ: قَالَ رَسُولُ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ: إِنَّ الْمُسْلِمَ إِذَا صَافَحَ أَخَاهُ تَحَاتَّتْ خَطَايَاهُمَا كَمَا يَتَحَاتُّ وَرَقُ الشَّجَرِ

1. Abu Huraira Radhiyallahu anhu akusiudza kuti : mtumiki wathu Muhammad sallalahu Alayhi wasallam adanena kuti, ” ndithudi msilamu akakumana ndi msilamu mzake ndikugwirana Manga akulonjerana ndichimwemwe, zotsathira zake ndizakuti Mulungu Allah Taala amawakululukira matchimo awo ndi masamba amagwera mmitengo.

Ahadith ikupezeka : musnad al-Bazzar 8335, al-Targheeb 3:433.

عَنْ الْبَرَاءِ بْنِ عَازِبٍ قَالَ: قَالَ رَسُولُ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ: مَا مِنْ مُسْلِمَيْنِ يَلْتَقِيَانِ فَيَتَصَافَحَانِ إِلَّا غُفِرَ لَهُمَا قَبْلَ أَنْ يَفْتَرِقَا

2. Al-bara ‘ ibn Azib Radhiyallahu Anhu akusiudza kuchokera Kwa mtumiki wathu Muhammad sallalahu Alayhi wasallam kuti : sizingatheke msilamu ndi mnzake akakumana ndikugwirana manja akulonjerana wina ndi mnzake pokapoka atakululukilidwa matchimo awo asadasiyane pamalopo.

Ahadith ikupezeka sunan al- Tirmidhi 2727

 

عَنْ أَنَسٍ: قَالَ: كَانَ أَصْحَابُ النَّبِيِّ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ إِذَا تَلَاقَوْا تَصَافَحُوا، وَإِذَا قَدِمُوا مِنْ سَفَرٍ تَعَانَقُوا

3 Anas ibn Malik Radhiyallahu Anhu akusiudza kuti chinali chizolowedzi omutsatira mtumiki sallalahu Alayhi wasallam masahaba ngati akumana wina ndi mnzake amagwirana manja komanso ngati akuchokera pa ulendo amakumbatilana wina ndi mnzake

Ahadith ikupezeka Al-mu’jam al-Awsat 97,al-Targheeb 3:433

Ife tili ndizambiri zoti tingamatsatire tiyenera kuchita kenakake kuti tidutse Nthawi imeneyi cholinga chathu lero chisakhale choononkha m’badwe omwe ukubwera kutsogolo kuno. Kodi tiwaonetsa zochita zathu ana athu mmene tikuithawira sunna ya mtumiki wathu sallalahu Alayhi wasallam? Kapena tiyisiya sunna ya mtumiki sallalahu Alayhi wasallam Kwa zizukulu zathu kapena m’badwe ukubwera kutsogolo kuno. Tili ndi mwayi oti tiwaudze ana athu makhalidwe amtumiki Muhammad sallalahu Alayhi wasallam. Tiwaphuzitse Ana athu za njira ya mtumiki sallalahu Alayhi wasallam.

Ndi mwayi oti kukumana ndi mtumiki wathu Muhammad sallalahu Alayhi wasallam ndiponso ndingakamuudze kuti tinagwira njira yake, pomwe anthu ozungulira Ife amkati kuisatira sunna ndi chiphinjo kwambiri.

Mulungu Allah Taala atilemekedzeke Ife ndikugwirana manja pamodzi poitetedza njira imeneyi ya mtumiki Muhammad sallalahu Alayhi wasallam.