Home / Languages / Chichewa / ANA: CHIKHULUPILITSO CHACHIKULU – CHICHEWA TRANSLATION OF “CHILDREN, A GREAT TRUST”

ANA: CHIKHULUPILITSO CHACHIKULU – CHICHEWA TRANSLATION OF “CHILDREN, A GREAT TRUST”

” Eee inu amene mwakhulupilira,zitetezeni nokha pamodzi ndi mabanja anu Ku ng’anjo ya moto umene nkhuni zake ndi anthu komanso miyala,omwe ayang’aniri ake ndi Angelo owoopsa ndi amphamvu,ndipo samanyonzera zomwe Allah awalamura,iwo amachita zomwe Allah awalamura (Al-qur’an 66/6).

Mthenga wa Allah madalitso ndi mtendere zipite kwa iye adati; “Mwana ariyense pobadwa nchilengedwe chake amabadwa ali nsilamu,koma makolo ake pamalo omwe wabadwirapo ndi omwe amamusintha kumpanga akhale muyuda,mkhirisitu, kapena opembedza Moto.(Bukhari 1385)

Ana ndi Chokhulupilitsa chochokera kwa Allah,kotero kuteteza Imaan yawo ndi chipembedzo chawo ukhale udindo waukulu wa tonsefe.
Makhalidwe akuchitika nsukulu zambiri panopa ndi chiopsezo cha ana kumbali ya Imaan yawo komanso chipembedzo chawo.Panopa kukula Kwa maphunziro ophunzisa ana mmasukulu zosemphana ndi chipembedzo cha chisilamu nkwachidziwikire.Udindo wa kholo lililonse ndikuyang’anira ndinso Kuika patsogolo njira yotetezera Imaan ndi chipembedzo cha ana ake.
Ana osalakwa komanso osachimwa sakuyenera akhale Malo omwe angachotse Imaan yawo komanso umunthu kapena kuzisunga kwawo.Zisafike poti mpaka tsiku lotsiriza ana akakhale akulimbana kukangana ndi makolo awo.
Allah Ta’ala watenga udindo opereka Mariziq (zofunika pamoyo wa zolengedwa).Palibe nzimu omwe udzafe osalandira gawo lake lomwe lidaikidwa.
Kuwuopa kwambiri umphawi ndi chida chomwe satana akuchigwilisira ntchito powononga Imaan(Chikhulupiliro) chathu.

” Satana akukuopsezani ndi umphawi ndikukulamurani kuchita zinthu zosalungama (Al-Qur’an 2/268)

Choncho pakufunika kuchilimikira kuwateteza ana athu pambalanganda a malo omwe ali oipa.Mmene kungathekere Makolo akulimbikisidwa kuwaphunzitsira ana mmanyumba.Sikuti ichi ndi chinthu chosatheka.Allah Ta’ala apanga kuthekera Kwa omwe ayikire Chikhulupiliro cha chithandizo chake cha Allah.
Pophatikiza kuteteza ana athu mmalo oyipa omwe akupezeka, kuchilimikira kukufunika kukhalepo powaphunzisa ana athu Chikhulupiliro chowona cheni cheni,ndi zofunikira za chipembedzo,ndinso kakhalidwe Ka chisilamu.

Pamene tikutumiza ana kukaphunzira Ku madarasa kholo lililonse likhale ndi chidwi kuyang’anitsitsa mmene mwana akupitira chitsogolo ndi maphunziro ake.

Madarasa ndi nchilikizo okhawo wa mwana pa maphunziro ake a chipembedzo.Pakufunika kusamala kuonetsetsa kuti mwana akuphunzisidwa ndi M’phunzitsi odalilika ndi owopa Allah.Kupanda kutero maphunziro omwe angaphunzire kungokhala kudziwa zinthu zoti sizingapereke kusintha kulikonse ngakhalenso phindu.

Zifukwa zosamveka bwino ndi zosakwanira zisasekeleredwe kapena kuloledwa kuti mpaka mwana asapite kukaphunzira Ku Madarasa.Ana athu akupangidwa kuti azimvetsetsa kufunikira kophunzira zofunikira pa moyo.Zoona zake ndizoti nkofunikira kwambiri kuti tidzale ndi kukhazikitsa mwa ana athu kufunikira Kwa maphunziro a chipembedzo cha chisilamu omwe ndi gwelo la chipambano chosatha ku moyo wa padziko lapansi pano komanso pambuyo pa moyo uno(Aakhira).

Mongozembera ndekuti Makolo omwenso sakulora mwana wawo kusiya maphunziro ongopeza zofuna zadziko lapansi lokha ndekuti akumulora mwana wawo kusiya maphunziro a dini (Madarasa).

” Mthenga wa Allah madalitso ndi mtendere zipite Kwa iye adati: ariyense mwa inu ndi m’busa, ariyense azafunsidwa za nkhosa zake “(Bukhari 893).

Timpemphe Allah Ta’ala kuti atipase kuthekera koti tithe kuteteza Chokhulupilira (Amaana) chomwe Allah adatipatsa (omwe ndi ana)kuti tiwayang’anire,ndinso tithe kuteteza Imaan ,ndi chipembedzo cha ana athu kufikira mpaka tsiku lachimalizo.Amin

14 Jumadal Ãkhirah 1443/16 January 2022 A0027

For PDF, click here:

ANA. CHIKHULUPILITSO CHACHIKULU

 

DOWNLOAD